11 Ndidzaleketsanso kusekerera kwace konse, madyerero ace, pokhala mwezi pace, ndi masabata ace, ndi masonkhano ace onse oikika.
12 Ndipo ndidzapasula mipesa yace ndi mikuyu yace, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama zakuthengo zidzaidya.
13 Ndipo ndidzamlanga cifukwa ca masiku a Abaala amene anawafukizira, nabvala mphete za m'mphuno, ndi zokometsera zace, natsata omkonda, nandiiwala Ine, ati Yehova.
14 Cifukwa cace taonani, ndidzamkopa ndi kumka naye kucipululu, ndi kulankhula naye momkonda mtima.
15 Ndipo ndidzampatsa minda yace yamphesa kuyambira pomwepo, ndi cigwa ca Akori cikhale khomo la ciyembekezo; ndipo adzabvomereza pomwepo monga masiku a ubwana wace, ndi monga tsiku lokwera iye kuturuka m'dziko la Aigupto.
16 Ndipo kudzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, udzandicha Mwamuna wanga, osandichanso Baala wanga.
17 Pakuti ndidzacotsa maina a Abaala m'kamwa mwace; ndipo silidzakumbukikanso dzina lao.