3 Ndinafuna mumtima mwanga kusangalatsa thupi langa ndi vinyo, mtima wanga ulikunditsogolera mwanzeru, ndi kugwira utsiru, kuti ndizindikire cabwinoco ca ana a anthu nciani cimene azicicita pansi pa thambo masiku onse a moyo wao.
4 Ndinadzipangira zazikuru; ndinadzimangira nyumba; ndi kunka mipesa;
5 ndinakonza mphanie ndi minda yanga, ndi kuokamo mitengo ya zipatso za mitundu mitundu;
6 ndinadzipangira ndekha matamanda a madzi akuthirira madzi m'nkhalango momeramo mitengo;
7 ndinadzitengera akapolo ndi adzakazi, ndinali ndi akapolo anabadwa kwanga; ndinalemeranso pokhala nazo zoweta zazikuru ndi zazing'ono kupambana onse anakhala m'Yerusalemu ndisanabadwe ine;
8 ndinakundikanso siliva ndi golidi ndi cuma ca mafumu ndi madera a dziko; ndinaitanitsa amuna ndi akazi akuyimba ndi zokondweretsazo za ana a anthu, ndizo zoyimbira za mitundu mitundu.
9 Ndinakula cikulire kupambana onse anali m'Yerusalemu ndisanabadwe ine; ndipo nzeru yanganso inakhala nanebe.