1 Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala m'Yerusalemu kasupe wa kwa ucimo ndi cidetso.
2 Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzacotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wacidetso.
3 Ndipo kudzacitika, akaneneranso wina, atate wace ndi mai wace ombala adzanena naye, Sudzakhala ndi moyo, pakuti unena bodza m'dzina la Yehova; ndipo atate wace ndi mai wace ombala adzamgwaza ponenera iye.
4 Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo kuti aneneri adzacita manyazi yense ndi masomphenya ace, ponenera iye; ndipo sadzabvala copfunda caubweya kunyenga naco;
5 koma adzati, Sindiri mneneri, ndiri wolima munda; pakuti munthu anandiyesa kapolo kuyambira ubwana wanga.
6 Ndipo wina akati kwa iye, Zipsera izi m'manja mwako nza ciani? adzayankha, Ndizo za mabala anandilasa m'nyumba ya ondikonda.
7 Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.