4 Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo kuti aneneri adzacita manyazi yense ndi masomphenya ace, ponenera iye; ndipo sadzabvala copfunda caubweya kunyenga naco;
5 koma adzati, Sindiri mneneri, ndiri wolima munda; pakuti munthu anandiyesa kapolo kuyambira ubwana wanga.
6 Ndipo wina akati kwa iye, Zipsera izi m'manja mwako nza ciani? adzayankha, Ndizo za mabala anandilasa m'nyumba ya ondikonda.
7 Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.
8 Ndipo kudzacitika m'dziko lonse, ati Yehova, magawo awiri m'menemo adzalikhidwa nadzafa; koma gawo lacitatu lidzasiyidwa m'mwemo.
9 Ndi gawo lacitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golidi; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.