3 Pamenepo Yehova adzaturuka, nadzacita nkhondo ndi amitundu aja, monga anacitira nkhondo tsiku lakudumana.
4 Ndi mapazi ace adzaponda tsiku lomwelo pa phiri la Azitona, liri pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala cigwa cacikuru; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwela.
5 Pamenepo mudzathawa kudzera cigwa ca mapiri anga; pakuti cigwa ca mapiri cidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira cibvomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu.
6 Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, sikudzakhala kuunika, zowalazo zidzada;
7 koma lidzakhala tsiku la pa lokha lodziwika ndi Yehova; palibe usana, palibe usiku; koma kudzatero kuti madzulo kudzati mbe.
8 Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzaturuka ku Yerusalemu; gawo lao lina kumka ku nyanja ya kum'mawa, ndi gawo lina kumka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu.
9 Ndipo Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse; tsiku lomwelo Yehova adzakhala Iye yekha, ndi dzina lace ilo lokha.