10 Yimba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndirinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova.
11 Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.
12 Ndipo Yehova adzalandira colowa cace Yuda, ngati gawo lace m'dziko lopatulikalo, nadzasankhanso Yerusalemu.
13 Khalani cete, anthu onse, pamaso pa Yehova; pakuti wagalamuka mokhalira mwace mopatulika.