10 Ndipo ndidzaononga magareta kuwacotsa m'Efraimu, ndi akavalo kuwacotsa m'Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wace udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.
11 Iwenso, cifukwa ca mwazi wa pangano lako ndinaturutsa andende ako m'dzenje m'mene mulibe madzi.
12 Bwererani kudza kulinga, andende a ciyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera cowirikiza.
13 Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efraimu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi.
14 Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi mubvi wace udzaturuka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akabvumvulu a kumwela.
15 Yehova wa makamu adzawacinjiriza; ndipo adzadza, nadzapondereza miyala yoponyera; ndipo adzamva, nadzacita phokoso ngati avinyo; ndipo adzadzazidwa ngati mbale, ngati ngondya za guwa la nsembe.
16 Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ace; pakuti adzakhala ngati miyala ya m'korona yakunyezimira pa dziko lace.