1 Koma mutu wafzi tanenazi ndi uwu: Tiri naye Mkuruwansembe wotere, amene anakhala pa dzanja lamanja la mpando wacifumu wa Ukulu m'Kumwamba,
2 Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa cihema coona, cimene Ambuye anacimanga, si munthu ai.
3 Pakuti mkulu wa ansembe ali yense aikidwa kupereka mitulo, ndiponso nsembe; potero nkufunika kuti ameneyo akhale nako kanthunso kakupereka,
4 Ndipo iye akadakhala padziko, sakadakhala konse wansembe, popeza pali iwo akupereka mitulo monga mwa lamulo;