13 Koma kalonga wa ufumu wa Perisiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaeli, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Perisiya.
14 Ndadzera tsono kukuzindikiritsa codzagwera anthu a mtundu wako masiku otsiriza; pakuti masomphenyawo ndiwo a masiku a m'tsogolo.
15 Ndipo atanena ndi ine monga mwa mau awa, ndinaweramitsa nkhope yanga pansi ndi kukhala du.
16 Ndipo taonani, wina wakunga ana a anthu anakhudza milomo yanga; pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndi kunena naye woima popenyana nane, Mbuye wanga, cifukwa ca masomphenyawo zowawa zanga zandibwerera, ndipo ndiribenso mphamvu.
17 Pakuti mnyamata wa mbuye wanga inu akhoza bwanji kulankhula ndi mbuye wanga inu? pakuti ine tsopano apa mulibenso mphamvu mwa ine, osanditsaliranso mpweya.
18 Pamenepo anandikhudzanso wina, maonekedwe ace ngati munthu, nandilimbikitsa ine.
19 Nati, Munthu wokondedwatu iwe, Usaope, mtendere ukhale nawe; limbika, etu limbika. Ndipo pamene ananena ndi ine ndinalimbikitsidwa, ndinati, Anene mbuye wanga; pakuti mwandilimbikitsa.