16 Nalowa Danieli, nafunsa mfumu amuikire nthawi, kuti aululire mfumu kumasulira kwace.
17 Pamenepo Danieli anapita ku nyumba kwace, nadziwitsa anzace Hananiya, Misaeli, ndi Azariya, cinthuci;
18 kuti apemphe zacifundo kwa Mulungu wa Kumwamba pa cinsinsi ici; kuti Danieli ndi anzace asaonongeke pamodzi ndi eni nzeru ena a ku Babulo.
19 Pamenepo cinsinsico cinabvumbulutsidwa kwa Danieli m'masomphenya a usiku. Ndipo Danieli analemekeza Mulungu wa Kumwamba.
20 Danieli anayankha, nati, Lilemekezedwe dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi, a pakuti nzeru ndi mphamvu ziri zace;
21 pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, acotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi cidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira.
22 Iye abvumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye.