24 Pamenepo mfumu Nebukadinezara anadabwa, nauka msanga, nanena nati kwa mandoda ace, Kodi sitinaponya amuna atatu omangidwa m'kati mwa moto? Anayankha nati kwa mfumu, Inde mfumu.
25 Anayankha, nati, Taonani, ndirikuona amuna anai omasuka, alikuyenda m'kati mwa moto; ndipo alibe kuphwetekwa, ndi maonekedwe a wacinai akunga mwana wa milungu.
26 Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo la ng'anjo yotentha yamoto, analankhula, nati, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, inu atumiki a Mulungu Wam'mwambamwamba, turukani, idzani kuno. Pamenepo Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, anaturuka m'kati mwa moto.
27 Ndipo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, ndi mandoda a mfumu, atasonkhana, anaona amuna awa, kuti moto unalibe mphamvu pa matupi ao, losawauka tsitsi la pamutu pao, ndi zopfunda zao zosasandulika, pfungo lomwe lamoto losawaomba.
28 Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, amene anatuma mthenga wace, napulumutsa atumiki ace omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu wao wao.
29 Cifukwa cace ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uli wonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, adzadulidwa nthuli nthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.
30 Pamenepo mfumu inakuza Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, m'dera la ku Babulo.