15 Ndipo tsono anabwera nao kwa ine anzeru, openda, kuti awerenge lemba ilo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwace; koma sanakhoza kufotokozera kumasulira kwa cinthuci.
16 Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwace, udzabvekedwa cibakuwa, ndi unyolo wagolidi m'khosi mwako; nudzakhala wolamulira wacitatu m'ufumuwo.
17 Pamenepo anayankha Danieli, nati kwa mfumu, Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphotho zanu mupatse wina; koma ndidzawerengera mfumu lembalo, ndi kumdziwitsa kumasulira kwace.
18 Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi cifumu;
19 ndipo cifukwa ca ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, a manenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pace; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.
20 Koma pokwezeka mtima wace, nulimba mzimu wace kucita modzikuza, anamtsitsa pa mpando wa ufumu wace, namcotsera ulemerero wace;
21 ndipo anamuinga kumcotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wace unasandulika ngati wa nyama za kuthengo, ndi pokhala pace mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lace linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, nauikira ali yense Iye afuna mwini.