5 Nthawi yomweyo zinabuka zala za dzanja la munthu, nizinalemba pandunji pa coikapo nyali, pomata pa khoma la cinyumba ca mfumu; ndipo mfumu inaona nsonga yace ya dzanja lidalembalo.
6 Pamenepo padasandulika pa nkhope pace pa mfumu, ndi maganizo ace anamsautsa, ndi mfundo za m'cuuno mwace zinaguruka, ndi maondo ace anaombana.
7 Nipfuulitsa mfumu abwere nao openda, Akasidi, ndi alauli, Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babulo, Ali yense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwace, adzabvekedwa cibakuwa, ndi unyolo wagolidi m'khosi mwace, nadzakhala wolamulira wacitatu m'ufumuwu.
8 Pamenepo analowa anzeru onse a mfumu, koma sanakhoza kuwerenga lembalo, kapena kudziwitsa mfumu kumasulira kwace.
9 Ndipo mfumu Belisazara anabvutika kwambiri, ndi nkhope yace inasandulika, ndi akuru ace anathedwa nzeru.
10 Cifukwa ca mau a mfumu ndi akuru ace mkazi wamkuru wa mfumu analowa m'nyumba ya madyerero; mkazi wa mfumu ananena, nati, Mfumu, mukhale ndi moyo kosatha; asakubvuteni maganizo anu, ndi nkhope yanu isasandulike;
11 pali munthu m'ufumu mwanu mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera; ndipo masiku a atate wanu munapezeka mwa iye kuunika, ndi luntha, ndi nzeru, ngati nzeru ya milungu; ndipo mfumu Nebukadinezara atate wanu, inde mfumu atate wanu anamuika akhale mkuru wa alembi, openda, Akasidi, ndi alauli;