1 Kudamkomera Dariyo kuikira ufumuwo akalonga zana limodzi mphambu makumi awiri akhale m'madera onse a ufumu;
2 ndi akuyang'anira iwo akulu atatu, woyamba wao ndi Danieli; kuti akalonga awa adziwerengere kwa iwo, ndi kuti za mfumu zisasoweke.
3 Pamenepo Danieli amene anaposa akuluwa ndi akalonga, popeza munali mzimu wopambana mwa iye, ndi mfumu inati imuike woyang'anira ufumu wonse.
4 Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola cifukwa Danieli, kunena za ufumuwo; koma sanakhoza kupeza cifukwa kapena colakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo sanaona cosasamala kapena colakwa ciri conse mwa iye.
5 Pamenepo anthu awa anati, Sitidzamtola cifukwa ciri conse Danieli amene, tikapanda kumtola ici pa cilamulo ca Mulungu wace.
6 Ndipo akuru awa ndi akalonga anasonkhana kwa mfumu mofulumira, natero nayo, Mfumu Dariyo, mukhale ndi moyo cikhalire.