11 Pamenepo anasonkhana anthu awa, napeza Danieli alikupemphera ndi kupembedza pamaso pa Mulungu wace.
12 Ndipo anayandikira, nanena pamaso pa mfumu za coletsaco ca mfumu, Kodi simunatsimikiza coletsaco, kuti ali yense akapempha kanthu kwa mulungu ali yense, kapena kwa munthu ali yense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango? Mfumu niyankha, niti, Coona cinthuci, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika.
13 Pamenepo anayankha, nati pamaso pa mfumu, Danieli uja wa ana a ndende a Yuda sasamalira inu, mfumu, kapena coletsa munacitsimikizaco; koma apempha pemphero lace katatu tsiku limodzi.
14 Ndipo mfumu m'mene atamva mau awa anaipidwa kwambiri, naika mtima wace pa Danieli kuti amlanditse, nayesetsa mpaka polowa dzuwa kumlanditsa.
15 Koma anthu awa anasonkhana kwa mfumu, nati kwa mfumu, Dziwani, mfumu, kuti lamulo la Amedi ndi Aperisi, ndilo kuti coletsa ciri conse ndi lemba liri lonse idazikhazikira mfumu, zisasinthike.
16 Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Danieli, namponya m'dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Danieli, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.
17 Ndipo anatenga mwala, nauika pakamwa pa dzenje, niukomera mfumu ndi cosindikizira cace, ndi cosindikizira ca akuru ace, kuti kasasinthike kanthu ka Danieli.