16 Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za coonadi za ici conse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwace kwa zinthuzi:
17 Zirombo zazikuru izi zinai ndizo mafumu anai amene adzauka pa dziko lapansi.
18 Koma opatulika la Wam'mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, ku nthawi zomka muyaya.
19 Pamenepo ndinafuna kudziwa coonadi ca cirombo cacinai cija cidasiyana nazo zonsezi, coopsa copambana, mano ace acitsulo, ndi makadabo ace amkuwa, cimene cidalusa, ndi kuphwanya, ndi kupondereza zotsala ndi mapazi ace;
20 ndi za nyanga khumi zinali pamutu pace, ndi nyanga yina Idaphukayi, imene zidagwa zitatu patsogolo pace; nyangayo idali ndi maso ndi pakamwa pakunena zazikuru, imene maonekedwe ace anaposa zinzace.
21 Ndinapenya, ndipo nyanga yomweyi inacita nkhondo ndi opatulikawo, niwalaka, mpaka inadza Nkhalamba ya kale lomwe;
22 ndi mlandu unakomera opatulika a Wam'mwambamwamba, nifika nthawi yakuti ufumu unali wao wa opatulikawo.