1 Caka coyamba ca Dariyo mwana wa Ahaswero, wa mbeu ya Amedi, amene anamlonga mfumu ya Akasidi;
2 caka coyamba ca ufumu wace, ine Danieli ndinazindikira mwa mabuku kuti ciwerengo cace ca zaka, cimene mau a Yehova anadzera naco kwa Yeremiya mneneri, kunena za makwaniridwe a mapasuko a Yerusalemu, ndizo zaka makumi asanu ndi awiri.
3 Ndipo ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu, kumfunsa Iye m'pemphero, ndi mapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa.
4 Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kubvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkuru ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi cifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu,