18 Mulungu wanga, cherani khutu, nimumvere, tsegulani maso anu, nimupenye zopasuka zathu, ndi mudzi udachedwawo dzina lanu; pakuti sititula mapembedzero athu pamaso panu, cifukwa ca nchito zathu zolungama, koma cifukwa ca zifundo zanu zocuruka.
19 Ambu ye, imvani; Ambuye, khululukirani; Ambuye, mverani nimucite; musacedwa, cifukwa ca inu nokha, Mulungu wanga; pakuti mudzi wanu ndi anthu anu anachedwa dzina lanu.
20 Ndipo pakunena ine, ndi kupemphera, ndi kubvomereza cimo langa, ndi cimo la anthu amtundu wanga Israyeli, ndi kutula cipembedzero canga pamaso pa Yehova Mulungu wanga, cifukwa ca phiri lopatulika la Mulungu wanga;
21 inde pakunena ine m'kupemphera, munthu uja Gabrieli, amene ndidamuona m'masomphenya poyamba paja, anauluka mwaliwiro nandikhudza ngati nthawi yakupereka nsembe ya madzulo.
22 Ndipo anandilangiza ine, ndi kulankhula nane, nati, Danieli iwe, ndaturuka tsopano ine kukuzindikiritsa mwaluntha.
23 Pakuyamba iwe mapembedzero ako, linaturuka lamulo; ndipo ndadza ine kukufotokozera; pakuti ukondedwa kwambiri; zindikira tsono mau awa, nulingirire masomphenyawo.
24 Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu amtundu wako ndi mudzi wako wopatulika, kumariza colakwaco, ndi kutsiriza macimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa cilungamo cosalekeza, ndi kukhomera cizindikilo masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulikitsa.