3 Ndipo ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu, kumfunsa Iye m'pemphero, ndi mapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa.
4 Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kubvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkuru ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi cifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu,
5 tacimwa, tacita mphulupulu, tacita zoipa, tapanduka, kupambuka ndi kusiya maneno anu ndi maweruzo anu;
6 sitinamvera atumiki anu aneneri, amene ananena m'dzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu, ndi anthu onse a m'dziko.
7 Ambuye, cilungamo nca Inu, koma kwa ife manyazi a nkhope yathu, monga lero lino; kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, ndi kwa Aisrayeli onse okhala pafupi ndi okhala kutali, ku maiko onse kumene mudawaingira, cifukwa ca kulakwa kwao anakulakwirani nako.
8 Ambuye, kwa ife kuli manyazi a nkhope yathu, kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, ndi kwa makolo athu; pakuti takucimwirani.
9 Ambuye Mulungu wathu ndiye wacifundo, ndi wokhululukira; pakuti tampandukira Iye;