14 a pafupi naye ndiwo Karisena. Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena, ndi Memukana, akalonga asanu ndi awiri a Perisiya ndi Mediya, openya nkhope ya mfumu ndi kukhala oyamba m'ufumu.
15 Anati, Tidzacitanji naye mkazi wamkuru Vasiti monga mwa malamulo, popeza sanacita comuuza mfumu Ahaswero mwa adindo?
16 Ndi Memukana anati pamaso pa mfumu ndi akalonga, Vasiti mkazi wamkuru sanalakwira mfumu yekha, komanso akalonga onse, ndi mitundu yonse ya anthu okhala m'maiko onse a mfumu Ahaswero.
17 Pakuti macitidwe awa a mkazi wamkuruyo adzabuka kufikira akazi onse, kupeputsa amuna ao pamaso pao; anthu akati, Mfumu Ahaswero anati abwere naye Vasiti mkazi wamkuru pamaso pace, koma sanadza iye.
18 Inde tsiku lomwelo akazi akuru a Perisiya ndi Mediya, atamva macitidwe a mkazi wamkuruyo, adzatero nao momwemo kwa akalonga onse a mfumu. Ndi cipeputso ndi mkwiyo zidzacuruka.
19 Cikakomera mfumu, aturuke mau acifumu pakamwa pace, nalembedwe m'malamulo a Aperisiya ndi Amediya, angasinthike, kuti Vasiti asalowenso pamaso pa mfumu Ahaswero; ndi mfumu aninkhe cifumu cace kwa mnzace womposa iye.
20 Ndipo mau amene adzaika mfumu akamveka m'ufumu wace wonse, (pakuti ndiwo waukuru), akazi onse adzacitira amuna ao ulemu, akulu ndi ang'ono.