3 caka cacitatu ca ufumu wace, anakonzera madyerero akalonga ace onse, ndi omtumikira; amphamvu a Perisiya ndi Mediya, omveka ndi akalonga a maikowo anakhala pamaso pace,
4 pamene anaonetsa zolemera za ufumu wace waulemu, ndi ulemerero wa ukulu wace woposa, masiku ambiri, ndiwo masiku zana limodzi, mphambu makumi asanu ndi atatu.
5 Atatha masikuwa, mfumu inakonzera madyerero anthu onse okhala m'cinyumba ca ku Susani, akulu ndi ang'ono, masiku asanu ndi awiri, ku bwalo la munda wa maluwa wa ku cinyumba ca mfumu;
6 panali nsaru zolenjeka zoyera, zabiriwiri, ndi zamadzi, zomangika ndi zingwe za thonje labafuta, ndi lofiirira, pa zigwinjiri zasiliva, ndi nsanamira zansangalabwi; makama anali a golidi ndi siliva pa mayalidwe a miyala yofiira, ndi yoyera, ndi yoyezuka, ndi yakuda.
7 Nawapatsa cakumwa m'zomwera zagolidi, zomwerazo nzosiyana-siyana, ndi vinyo wacifumu anacuruka, monga mwa ufulu wa mfumu.
8 Ndi mamwedwewo anali monga mwa lamulo; panalibe kukakamiza; pakuti mfumu idaikira akulu onse a nyumba yace motero, kuti acite monga momwe akhumba ali yense.
9 Vasiti yemwe, mkazi wamkuru, anakonzera akazi madyerero m'nyumba yacifumu ya mfumu Ahaswero.