1 Koma podziwa Moredekai zonse zidacitikazi, Moredekai anang'amba zobvala zace, nabvala ciguduli ndi mapulusa, naturuka pakati pa mudzi, napfuula, nalira kulira kwakukuru ndi kowawa,
2 nafika popenyana ndi cipata ca mfumu; popeza sanathe munthu kulowa ku cipata ca mfumu wobvala ciguduli.
3 Ndi m'maiko monse, pali ponse anafikapo mau a mfumu ndi lamulo lace, panali maliro akuru mwa Ayuda, ndi kusala, ndi kulira misozi, ndi kubuma; nagona m'ciguduli ndi mapulusa ambiri.
4 Ndipo anamwali a Estere ndi adindo ace anadza, namuuza; ndi mkazi wamkuru anawawidwa mtima kwambiri, natumiza cobvala abveke Moredekai, ndi kumcotsera ciguduli cace; koma sanacilandira.
5 Pamenepo Estere anaitana Hataki mdindo wina wa mfumu, amene idamuika amtumikire, namuuza amuke kwa Moredekai, kuti adziwe ici nciani ndi cifukwa cace ninji.
6 Naturuka Hataki kumka kwa Moredekai ku khwalala la mudzi linali popenyana ndi cipata ca mfumu.