7 Ndipo Moredekai anamfotokozera zonse zidamgwera, ndi mtengo wace wa ndarama adati Hamani adzapereka m'nyumba ya cuma ca mfumu pa Ayuda, kuwaononga.
8 Anampatsanso citsanzo ca lamulo lolembedwa adalibukitsa m'Susani, kuwaononga, acionetse kwa Estere, ndi kumfotokozera, ndi kumlangiza alowe kwa mfumu, kumpembedza, ndi kupempherera anthu ace kwa iye.
9 Nadza Hataki, namuuza Estere mau a Moredekai.
10 Pamenepo Estere ananena ndi Hataki, namtuma akauze Moredekai, ndi kuti,
11 Akapolo onse a mfumu ndi anthu a m'maiko a mfumu adziwa kuti ali yense, ngakhale wamwamuna kapena wamkazi, akalowa kwa mfumu ku bwalo la m'katimo wosaitanidwa, lamulo la pa iye ndi limodzi, ndilo kuti amuphe, akapanda mfumu kumloza ndi ndodo yacifumu yagolidi kuti akhale ndi moyo; koma ine sanaodiitana ndilowe kwa mfumu masiku awa makumi atatu.
12 Ndipo anamuuza Moredekai mau a Estere.
13 Koma Moredekai anawauza ambwezere mau Estere, kuti, Usamayesa m'mtima mwako kuti udzapulumuka m'nyumba ya mfumu koposa Ayuda onse ena.