1 Ndipo kunali tsiku lacitatu, Estere anabvala zobvala zace zacifumu, nakaimirira m'bwalo la m'kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wace wacifumu m'nyumba yacifumu, pandunji polowera m'nyumba.
2 Ndipo kunali, pamene mfumu inaona Estere mkazi wamkuruyo alikuima m'bwalo, inamkomera mtima; ndi mfumu inamloza Estere ndi ndodo yacifumu yagolidi inali m'dzanja lace. Nayandikira Estere, nakhudza nsonga ya ndodoyo.
3 Ninena naye mfumu, Mufunanji, Estere mkazi wamkuru? pempho lanu nciani? lidzaperekedwa kwa inu, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.
4 Ndipo Estere anati, Cikakomera mfumu, adze mfumu ndi Hamani lero ku madyerero ndinawakonzera.
5 Niti mfumu, Mumfulumize Hamani, acitike mau a Estere. Nidza mfumu ndi Hamani ku madyerero adawakonzera Estere.
6 Ndipo mfumu inati kwa Estere pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nciani? lidzaperekedwa kwa inu; mufunanji? cidzacitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.