10 Ndipo analembera m'dzina la mfumu Ahaswero, nasindikiza ndi mphete ya mfumu, natumiza akalata ndi amtokoma pa akavalo, okwera pa akavalo aliwiro acifumu, obadwa mosankhika;
11 m'menemo mfumu inalola Ayuda okhala m'midzi iri yonse asonkhane, ndi kulimbikira moyo wao, kuononga, kupha, ndi kupulula mphamvu yonse ya anthu ndi ya dziko yofuna kuwathira nkhondo, iwo, ana ang'ono ao, ndi akazi ao, ndi kulanda zofunkha zao,
12 tsiku lomwelo, m'maiko onse a mfumu Ahaswero, tsiku lakhumi ndi citatu la mwezi wakhumi ndi ciwiri, ndiwo mwezi wa Adara.
13 Citsanzo cace, ca lemboli, cakuti abukitse lamulo m'maiko onse, cinalalikidwa kwa mitundu yonse ya anthu, kuti, Ayuda akonzekeretu tsiku lijalo, kubwezera cilango adani ao.
14 Naturuka amtokoma okwera pa akavalo aliwiro acifumu; pakuti mau a mfumu anawafulumiza ndi kuwaumiriza; ndipo lamulolo linabukitsidwa m'cinyumba ca ku Susani.
15 Ndipo Moredekai anaturuka pamaso pa mfumu wobvala cobvala cacifumu camadzi ndi coyera, ndi korona wamkuru wagolidi, ndi maraya abafuta ndi ofiirira; ndi mudzi wa Susani unapfuula ndi kukondwera.
16 Ayuda anali nako kuunika, ndi kukondwera, ndi cimwemwe, ndi ulemu.