Estere 8:4-10 BL92

4 Ndipo mfumu inaloza Estere ndi ndodo yacifumu yagolidi. Nanyamuka Estere, naima pamaso pa mfumu.

5 Nati, Cikakomera mfumu, ndipo ngati yandikomera mtima, niciyenera kwa mfumu, ngatinso ndimcititsa kaso, alembere cosintha mau a akalata a ciwembu ca Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, amene adawalembera kuononga Ayuda okhala m'maiko onse a mfumu;

6 pakuti ndidzapirira bwanji pakuciona coipa cirikudzera amtundu wanga, kapena ndidzapirira bwanji pakuciona cionongeko ca pfuko langa?

7 Pamenepo mfumu Ahaswero anati kwa mkazi wamkuru Estere, ndi kwa Moredekai Myuda, Taonani, ndampatsa Estere nyumba ya Hamani, ndi iyeyu anampacika pamtanda, cifukwa anaturutsa dzanja lace pa Avuda,

8 Mulembere inunso kwa Ayuda monga mufuna, m'dzina la mfumu, nimusindikize ndi mphete ya mfumu; pakuti kalata wolembedwa m'dzina la mfumu, ndi kusindikizika ndi mphete ya mfumu, palibe munthu akhoza kumsintha.

9 Pamenepo anaitana alembi a mfumu nthawi yomweyo, mwezi wacitatu, ndiwo mwezi wa Sivani, tsiku lace la makumi awiri ndi citatu, monga mwa zonse Moredekai analamulira; nalembera kwa Ayuda ndi kwa akazembe, ndi ziwanga, ndi akalonga a kumaiko, oyambira ku Indiya, ofikira ku Kusi, maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri, ku dziko liri lonse monga mwa cilembedwe cao, ndi mtundu uli wonse monga mwa cinenedwe cao, ndi kwa Ayuda monga mwa cilembedwe cao, ndi monga mwa cinenedwe cao.

10 Ndipo analembera m'dzina la mfumu Ahaswero, nasindikiza ndi mphete ya mfumu, natumiza akalata ndi amtokoma pa akavalo, okwera pa akavalo aliwiro acifumu, obadwa mosankhika;