6 Usalole m'kamwa mwako mucimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako cifukwa ninji, naononge nchito ya manja ako?
7 Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zacabe motero mocuruka mau; koma dziopa Mulungu.
8 Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kucotsa cilungamo ndi ciweruzo mwaciwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkuru wopambana asamalira; ndipo alipo akuru ena oposa amenewo.
9 Phindutu la dziko lipindulira onse; ngakhale mfumu munda umthandiza.
10 Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda cuma sadzakhuta phindu; icinso ndi cabe.
11 Pocuruka katundu, akudyapo acurukanso; nanga apindulira eni ace ciani, koma kungopenyera ndi maso ao?
12 Tulo ta munthu wogwira nchito ntabwino, ngakhale adya pang'ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.