1 Pakuti zonsezi ndinazisunga mumtima ndikalondoletu zonsezi; kuti olungama ndi anzeru ndi nchito zao ali m'manja a Mulungu; ngakhale kukonda ngakhale kudana anthu sadziwa; zonse ziri m'tsogolo mwao.
2 Zonse zigwera onse cimodzimodzi; kanthu kamodzi kangogwera wolungama ndi woipa; ngakhale wabwino ndi woyera ndi wodetsedwa: ngakhale wopereka nsembe ndi wosapereka konse; wabwino alingana ndi wocimwa; wolumbira ndi woopa lumbiro.
3 Ici ndi coipa m'zonse zicitidwa pansi pano, cakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udio, ndipo misala iri m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.
4 Pakuti woyang'ana ndi amoyo onse ali naco ciyembekezo; pakuti garu wamoyo aposa mkango wakufa.
5 Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.
6 Cikondi cao ndi mdano wao ndi dumbo lao lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kali konse kacitidwa pansi pano.
7 Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wabvomerezeratu zocita zako.