24 Halohesi, Pila, Sobeki,
25 Rehumu, Hasabina, Maaseya,
26 ndi Ahiya, Hanani, Anani,
27 Maluki, Harimu, Baana.
28 Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oyimbira, Anetini, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m'dziko kutsata cilamulo ca Mulugu, akazi ao, ana ao amuna ndi akazi, yense wodziwa ndi wozindikira,
29 amenewa anaumirira abale ao, omveka ao, nalowa m'temberero ndi lumbiro, kuti adzayenda m'cilamulo ca Mulungu anacipereka Mose mtumiki wa Mulungu, ndi kuti adzasunga ndi kucita zonse atilamulira Yehova Ambuye wathu, ndi maweruzo ace, ndi malemba ace;
30 ndi kuti sitidzapereka ana athu akazi kwa mitundu ya anthu a m'dziko, kapena kutengera ana athu amuna ana ao akazi;