1 Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu M-arabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaika zitseko pazipata);
2 anatumiza mau kwa ine Sanibalati ndi Gesemu, kuti, Tiyeni tikomane ku midzi ya ku cigwa ca Ono; koma analingirira za kundicitira coipa.
3 Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndirikucita nchito yaikuru, sindikhoza kutsika; ndiidulirenji padera nchito poileka ine, ndi kukutsikirani?
4 Nanditumizira ine mau otere kanai; ndinawabwezeranso mau momwemo.
5 Pamenepo Sanibalati anatuma mnyamata wace kwa ine kacisanu, ndi kalata wosatseka m'dzanja mwace;
6 m'menemo mudalembedwa, Kwamveka mwa amitundu, ndi Gasimu acinena, kuti iwe ndi Ayuda mulikulingirira za kupanduka; cifukwa cace mulikumanga lingali; ndipo iwe udzakhala mfumu yao monga mwa mau awa.
7 Ndiponso waika aneneri akubukitsa za iwe ku Yerusalemu, ndi kuti, Ku Yuda kuli mfumu, ndipo zidzamveka kwa mfumu, kuti kuli zotere. Tiyeni tsono tipangane pamodzi.
8 Koma ndinamtumizira mau, akuti, Palibe zinthu zotere zonga unenazi, koma uzilingirira mumtima mwako.
9 Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka nchito, ndipo siidzacitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.
10 Pamenepo ndinalowa m'nyumba ya Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, wobindikizidwayo, ndipo anati, Tikomane ku nyumba ya Mulungu m'kati mwa Kacisi, titsekenso pa makomo a Kacisi; pakuti akudza kudzapha iwe, inde akudza usiku kudzapha iwe.
11 Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? ndani wonga ine adzalowa m'Kacisi kupulumutsa moyo wace? sindidzalowamo.
12 Ndipo ndinazindikira kuti sanamtuma Mulungu; koma ananena coneneraco pa ine, popeza Tobiya ndi Sanibalati adamlembera.
13 Anamlembera cifukwa ca ici, kuti ine ndicite mantha, ndi kucita cotero, ndi kucimwa; ndi kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza.
14 Mukumbukile, Mulungu wanga, Tobiya ndi Sanibalati monga mwa nchito zao izi, ndi Nowadiya mneneri wamkazi yemwe, ndi aneneri otsala, amene anafuna kundiopsa.
15 Ndipo linga linatsirizika pa tsiku la makumi awiri ndi lacisanu la mwezi wa Eluli, titalimanga masiku makumi asanu mphambu awiri.
16 Ndipo kunali atacimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti nchitoyi inacitika ndi Mulungu wathu.
17 Masikuwo aufulu a Yuda analemberanso akalata ambiri kwa Tobiya; ndipo anawafikanso akalata ace a Tobiya.
18 Pakuti ambiri m'Yuda analumbirirana naye cibwenzi; popeza ndiye mkamwini wace wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wace Yehohanana adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.
19 Anachulanso nchito zace zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza akalata kuti andiopse ine.