1 Ndipo atatha kumanga linga, ndinaika zitseko, nakhazika odikira, ndi oyimbira, ndi Alevi;
2 ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.
3 Ndinanenanso nao, Asatsegule pa zipata za Yerusalemu lisanafunde dzuwa; ndi poimirira odikira atseke pazipata, nimuzipiringidze, nimuike alonda mwa iwo okhala m'Yerusalemu, yense polindirira pace, yense pandunji pa nyumba yace.
4 Mudziwo tsono ndi wacitando, ndi waukuru; koma anthu anali m'mwemo ngowerengeka, nyumba zomwe sizinamangike.
5 Ndipo Mulungu wanga anaika m'mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufuru, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa cibadwidwe cao. Ndipo ndinapeza buku la cibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m'mwemo.
6 Ana a dziko amene anakwera kucokera kundende a iwo adatengedwa ndende, amene Nebukadinezara mfumu ya Babulo adawatenga, anabwera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, yense ku mudzi wace, ndi awa:
7 ndiwo amene anadza ndi Zerubabele: Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Moredekai, Bilisani, Misiperete, Bigivai, Nehumu, Baana. Mawerengedwe a amuna a anthu Aisrayeli ndiwo:
8 ana a Parosi zikwi ziwiri mphambu zana limodzi kudza makumi asanu ndi awiri.
9 Ana a Sefatiya, mazana atatu mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.
10 Ana a Ara, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.
11 Ana a Pakati Moabu, a ana a Yesuwa ndi Yoabu, zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi atatu kudza khumi limodzi ndi asanu ndi atatu.
12 Ana a Elamu, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri ndi makumi asanu kudza anai.
13 Ana a Zatu, mazana asanu ndi atatu mphambu makumi anai kudza asanu.
14 Ana a Zakai, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.
15 Ana a Binui, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza asanu ndi atatu.
16 Ana a Betai, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.
17 Ana a Azigadi, zikwi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi awiri ndi awiri.
18 Ana a Adonikamu, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi, kudza asanu ndi awiri.
19 Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi awiri.
20 Ana a Adini, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu.
21 Ana a Aberi, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi atatu.
22 Ana a Hasumu, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.
23 Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza anai.
24 Ana a Harifi, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.
25 Ana a Gibeoni, makumi asanu ndi anai kudza asanu.
26 Amuna a ku Betelehemu ndi ku Netofa, zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza asanu ndi atatu.
27 Amuna a ku Anatoti, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.
28 Amuna a ku Bete-Azimaveti, makumi anai kudza awiri.
29 Amuna a ku Kiriyati Yearimu, Kefiira, ndi Beeroti, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi anai kudza atatu.
30 Amuna a ku Rama ndi Geba, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza mmodzi.
31 Amuna a ku Mikimasi, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri.
32 Amuna a ku Betele ndi Ai, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu.
33 Amuna a ku Nebo winayo, makumi asanu kudza awiri.
34 Ana a Elamu winayo, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri ndi makumi asanu kudza anai.
35 Ana a Harimu, mazana atatu mphambu makumi awiri.
36 Ana a Yeriko, mazana atatu mphambu makumi anai kudza asanu.
37 Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza mmodzi.
38 Ana a Senaa, zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi anai kudza makumi atatu.
39 Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu.
40 Ana a Imeri, cikwi cimodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.
41 Ana a Pasuru, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi anai ndi asanu ndi awiri.
42 Ana a Harimu, cikwi cimodzi mphambu khumi limodzi kudza asanu ndi awiri.
43 A Levi: ana a Yesuwa, a Kadimiyeli, a ana a Hodeva, makumi asanu ndi awiri kudza anai.
44 Oyimbira: ana a Asafu, zana limodzi mphambu makumi anai kudza asanu ndi atatu.
45 Odikira: ana a Salumu, ana a Ateri, ana a Talimoni, ana a Akubu, ana a Hatita, ana a Sobai, zana limodzi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi atatu.
46 Anetini: ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,
47 ana a Kerosi, ana a Siya, ana a Padoni,
48 ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Salimai,
49 ana a Hanani, ana a Gideri, ana a Gahara,
50 ana a Reaya, ana a Rezini, ana a Nekoda,
51 ana a Gazamu, ana a Uza, ana a Paseya,
52 ana a Besai, ana a Meunimu, ana a Nefusesimu,
53 ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri,
54 ana a Baziliti, ana a Mehida, ana a Harisa,
55 ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema,
56 ana a Neziya, ana a Hatifa.
57 Ana a akapolo a Solomo: ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Perida,
58 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli,
59 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti Hazebaimu, ana a Amoni.
60 Anetini onse, ndi ana a akapolo a Solomo, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri.
61 Ndipo okwera kucokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, ndi awa; koma sanakhoza kuchula nyumba za makolo ao, kapena mbumba zao, ngati ali a Israyeli;
62 ana a Delaya, ana a Tobiya, ana a Nekoda, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza awiri.
63 Ndi a ansembe: ana a Hobaya, ana a Hokozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgileadi, nachedwa ndi dzina lao.
64 Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa cibadwidwe, koma osawapeza; potero anawayesa odetsedwa, nawacotsa ku nchito ya nsembe.
65 Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulikitsa, mpaka wauka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu.
66 Msonkhano wonse pamodzi ndiwo zikwi makumi anai ndi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi,
67 osawerenga akapolo ao amuna ndi akazi, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana atatu ndi makumi atatu kudza asanu ndi awiri; ndipo anakhala nao amuna ndi akazi oyimbira mazana awiri mphambu makumi anai kudza asanu ndi mmodzi.
68 Akavalo ao ndiwo mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu kudza asanu ndi mmodzi; nyuru zao mazana awiri mphambu makumi anai kudza zisanu
69 ngamira zao mazana anai mphambu makumi atatu kudza asanu aburu ao zikwi zisanu ndi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi awiri.
70 Ndipo ena a akuru a nyumba za makolo anapereka kunchito. Kazembeyo anapereka kucuma madariki agolidi cikwi cimodzi, mbale zawazira makumi asanu, maraya a ansembe makumi atatu.
71 Enanso a akuru a nyumba za makolo anapereka ku cuma ca nchitoyi, madariki agolidi zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya siliva zikwi ziwiri mphambu mazana awiri.
72 Zopereka za anthu otsala ndizo madariki agolidi zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya siliva zikwi ziwiri, ndi maraya a ansembe makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi awiri.
73 Nakhala m'midzi mwao ansembe, ndi Alevi, ndi odikira, ndi oyimbira, ndi anthu ena, ndi Anetini, ndi Aisrayeli onse.Utakhala tsono mwezi wacisanu ndi ciwiri ana a Israyeli anakhala m'midzi mwao.