1 Ndipo ansembe ndi Alevi amene anakwera ndi Zerubabele mwana wa Sealtiyeli, ndi Yesuwa, ndi awa: Seraya, Yeremiya, Ezara,
2 Amariya, Maluki, Hatusi,
3 Sekaniya, Rehumu, Meremoti,
4 Ido, Ginetoi, Abiya,
5 Miyamini, Maadiya, Biliga,
6 Semaya, ndi Yoyaribi, Yedaya,
7 Salu, Amoki, Hilikiya, Yedaya. Awa ndi akuru a ansembe ndi abale ao m'masiku a Yesuwa.
8 Ndi Alevi ndiwo Yesuwa, Binui, Kadimiyeli, Serebiya, Yuda, ndi Mataniya; iye ndi abale ace amatsogolera mayamiko.
9 Ndi Bakibukiya ndi Uni, abale ao, anawayang'anira maulonda.
10 Ndi Yesuwa anabala Yoyakimu, ndi Yoyakimu anabala Eliasibi ndi Eliasibi anabala Yoyada,
11 ndi Yoyada anabala Yonatani, ndi Yonatani, anabala Yaduwa.
12 Ndi m'masiku a Yoyakimu ansembe akulu a nyumba za makolo ndiwo: wa Seraya, Meraya; wa Yeremiya, Hananiya;
13 wa Ezara, Mesulamu; wa Amariya, Yehohanana;
14 wa Maluki, Yonatani; wa Sebaniya, Yosefe;
15 wa Harimu, Adina; wa Merayoti, Helikai;
16 wa Ido, Zekariya; wa Ginetoni, Mesulamu;
17 wa Abiya, Zikiri; wa Minyamini, wa Moadiya, Pilitai;
18 wa Biliga, Samura; wa Semaya, Yehonatani;
19 ndi wa Yoyaribi, Matani; wa Yedaya, Uzi;
20 wa Salai, Kalai; wa Amoki, Eberi;
21 wa Hilikiya, Hasabiya; wa Yedaya, Netaneli.
22 M'masiku a Ehasibi, Yoyada, Yohanana, ndi Yoduwa, Alevi analembedwa akuru a nyumba za makolo; ansembe omwe, mpaka ufumu wa Dariyo wa ku Perisiya.
23 Ana a Levi, akuru a nyumba za makolo, analembedwa m'buku la macitidwe, mpaka masiku a Yohanana mwana wa Eliasibu.
24 Ndi akuru a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyeli, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda.
25 Mataniya, ndi Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni, Akubi, ndiwo odikira akulonda pa nyumba za cuma ziri kuzipata.
26 Awa anakhala m'masiku a Yoyakimu mwana wa Yesuwa, mwana wa Yozadaki, ndi m'masiku a Nehemiya kazembe, ndi a Ezara wansembe mlembiyo.
27 Ndipo popereka linga la Yerusalemu anafunafuna Alevi m'malo mwao monse, kubwera nao ku Yerusalemu, kuti acite kuperekaku mokondwera, ndi mayamiko, ndi kuyimbira, ndi nsanje, zisakasa, ndi azeze.
28 Ana a oyimbirawo anasonkhana ocokera ku dziko lozungulira Yerusalemu, ndi ku midzi ya Anetofati,
29 ndi ku Betegiligala, ndi ku minda ya Geba ndi Azimaveti; popeza oyimbirawo adadzimangira midzi pozungulira Yerusalemu.
30 Ndipo ansembe ndi Alevi anadziyeretsa okha, nayeretsa anthu, ndi zipata, ndi linga.
31 Pamenepo ndinakwera nao akuru a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akuru oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kumka ku cipata ca kudzala;
32 ndi pambuyo pao anayenda Hosaya, ndi limodzi la magawo awiri a akuru a Yuda,
33 ndi Azariya, Ezara ndi Mesulamu,
34 Yuda, ndi Benjamini, ndi Semaya, ndi Yeremiya,
35 ndi ana ena a ansembe ndi malipenga: Zekariya mwana wa Yonatani, mwana wa Semaya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu,
36 ndi abale ace: Semaya, ndi Azareli, Milalai, Gilelai, Maai, Netaneli, ndi Yuda, Hanani, ndi zoyimbira za Davide munthu wa Mulungu; ndi Ezara mlembiyo anawatsogolera;
37 ndi ku cipata ca kucitsime, ndi kundunji kwao, anakwerera pa makwerero a mudzi wa Davide, potundumuka linga, popitirira pa nyumba ya Davide, mpaka ku cipata ca kumadzi kum'mawa.
38 Ndi gulu lina la oyamikira linamuka mokomana nao, ndi ine ndinawatsata, pamodzi ndi limodzi la magawo awiri la anthu palinga, napitirira pa nsanja ya ng'anjo, mpaka ku linga lacitando;
39 ndi pamwamba pa cipata ca Efraimu, ndi ku cipata cakale, ndi ku cipata cansomba, ndi nsanja ya Hananeli, ndi nsanja ya Hameya, mpaka ku cipata cankhosa; ndipo anaima ku cipata cakaidi.
40 Atatero, magulu awiriwo a iwo oyamikira anaima m'nyumba ya Mulungu, ndipo ine ndi limodzi la magawo awiri a olamulira pamodzi ndi ine;
41 ndi ansembe, Eliakimu, Maaseya, Minyamini, Mikaya, Elioenai, Zekariya, ndi Hananiya, ali nao malipenga;
42 ndi Maaseya, ndi Semaya, ndi Eleazara, ndi Uzi, ndi Yehohanana, ndi Malikiya, ndi Elamu, ndi Ezeri. Ndipo oyimbira anayimbitsa Yeziraya ndiye woyang'anira wao.
43 Ndipo anaphera nsembe zambiri tsiku lija, nasekerera; pakuti Mulungu anawakondweretsa ndi cimwemwe cacikuru; ndi akazi omwe ndi ana anakondwera; ndi cikondwerero ca Yerusalemu cinamveka kutali.
44 Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za cuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzi limodzi la magawo khumi, kulonga m'mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi cilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi lakuimirirako.
45 Ndipo iwo anasunga udikiro wa Mulungu wao, ndi udikiro wa mayeretsedwe; momwemonso oyimbira ndi odikira, monga mwa lamulo la Davide ndi la Solomo mwana wace.
46 Pakuti m'masiku a Davide ndi Asafu kalelo kunali mkuru wa oyimbira, ndi wa nyimbo zolemekeza ndi zoyamikira Mulungu.
47 Ndi Aisrayeli onse m'masiku a Zerubabele, ndi m'masiku a Nehemiya, anapereka magawo a oyimbira ndi odikira, monga mudafunika tsiku ndi tsiku; nawapatulira Alevi; ndi Alevi anawapatulira ana a Aroni.