1 Pamenepo Eliasibu mkuru wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ace ansembe, namanga cipata cankhosa; anacipatula, naika zitseko zace, inde anacipatula mpaka nsanja ya Mea, mpaka nsanja ya Hananeeli.
2 Ndi pambali pace anamanga amuna a ku Yeriko. Ndi pambali pao anamanga Zakuri mwana wa Imri.
3 Ndi cipata cansomba anacimanga ana a Hasenaa; anamanga mitanda yace, ndi kuika zitseko zace, zokowera zace, ndi mipingiridzo yace.
4 Ndi pambali pao anakonza Meremoti mwana wa Uliya, mwana wa Kozi. Ndi pambali pao anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele. Ndi pambali pao anakonza Zadoki mwana wa Baana.
5 Ndi pambali pao anakonza Atekoa; koma omveka ao sanapereka makosi ao ku nchito ya Mbuye wao.
6 Ndi cipata cakale anacikonza Yoyada mwana wa Paseya; ndi Mesulamu mwana wa Besodeya anamanga mitanda yace, ndi kuika zitseko zace, ndi zokowera zace, ndi mipingiridzo yace.
7 Ndi pambali pao anakonza Melatiya Mgibeoni, ndi Yadoni Mheronoti, ndi amuna a ku Gibeoni, ndi a ku Mizipa, wa ulamuliro wa ciwanga tsidya lino la mtsinje.
8 Pambali pace anakonza Uziyeli mwana wa Haraya, wa iwo osula golidi. Ndi padzanja pace anakonza Hananiya, wa iwo osanganiza zonunkhira; nalimbikitsa Yerusalemu mpaka linga lacitando.
9 Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkuru wa dera lina la dziko la Yerusalemu.
10 Ndi pambali pao anakonza Yedaya mwana wa Harumafi, pandunji pa nyumba yace. Ndi pambali pace anakonza Hatusi mwana wa Hasabineya.
11 Malikiya mwana wa Harimu, ndi Hasubi mwana wa Pahati-Moabu, anakonzal gawo lina, ndi nsanja ya ng'anjo.
12 Ndi pambali pace anakonza Salumu mwana wa Halohesi, mkuru wa dera lina la dziko la Yerusalemu, iye ndi ana ace akazi.
13 Cipata ca kucigwa anacikonza Hanini; ndi okhala m'Zanowa anacimanga, naika zitseko zace, zokowera zace, ndi mipiringidzo yace; ndiponso mikono cikwi cimodzi ca lingalo mpaka ku cipata ca kudzala.
14 Ndi cipata ca kudzala anacikonza Malikiya mwana wa Rekabu, mkuru wa dziko la Bete Hakeremu; anacimanga, naika zitseko zace, zokowera zace, ndi mipiringidzo yace.
15 Ndi cipata ca kukasupe anacikonza Saluni mwana wa Koli, Hoze mkuru wa dziko la Mizipa anacimanga, nacikomaniza pamwamba pace, naika zitseko zace, zokowera zace, ndi mipiringidzo yace; ndiponso linga la dziwe la Sela pa munda wa mfumu, ndi kufikira ku makwerero otsikira ku mudzi wa Davide.
16 Potsatizana naye anakonza Nehemiya mwana wa Azibuki, mkuru wa dera lace lina la dziko la Bete Zuri, mpaka malo a pandunji pa manda a Davide, ndi ku dziwe adalikumba, ndi ku nyumba ya amphamvu aja.
17 Potsatizana naye anakonza Alevi, Rehumu mwana wa Bani. Pambali pace anakonza Hasabiya mkuru wa dera lina la dziko la Keila, kukonzera dziko lace.
18 Potsatizana naye anakonza abale ao, Bavai mwana wa Henadadi, mkuru wa dera lina la dziko la Keila.
19 Ndi pa mbali pace Ezeri mwana wa Yesuwa, mkuru wa Mizipa, anakonza gawo lina, pandunji pokwerera ku nyumba yosungamo zida za nkhondo, popindirira linga.
20 Potsatizana naye Baruki mwana wa Zabai anafulumira kukonza gawo lina kuyambira popindirira mpaka ku khomo la nyumba ya Eliasibu mkuru wa ansembe.
21 Potsatizana naye Meremoti mwana wa Uliya mwana wa Hakozi anakonza gawo lina, kuyambira ku khomo la nyumba ya Eliasibu kufikira malekezero ace a nyumba ya Eliasibu.
22 Ndi potsatizana naye anakonza ansembe okhala kucidikha.
23 Potsatizana nao anakonza Benjamini ndi Hasubi pandunji pa nyumba pao, Potsatizana nao anakonza Azariya mwana wa Maseya mwana wa Ananiya pafupi pa nyumba yace.
24 Potsatizana naye Binui mwana wa Henadadi anakonza gawo lina, kuyambira ku nyumba ya Azariya kufikira popindirira kufikira kungondya.
25 Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene iri ku bwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi.
26 Koma Anetini okhala m'Ofeli anakonza kufikira ku malo a pandunji pa cipata ca kumadzi kum'mawa, ndi nsanja yosomphokayo,
27 Potsatizana nao Atekoa anakonza gawo lina, pandunji pa nsanja yaikuru yosomphoka ndi ku linga la Ofeli.
28 Kumtunda kwa cipata ca akavalo anakonza ansembe, yense pandunji pa nyumba yace.
29 Potsatizana nao anakonza Zadoki mwana wa Imeri pandunji pa nyumba yace. Ndi potsatizana naye anakonza Semaya mwana wa Sekaniya, wosunga cipata ca kum'mawa.
30 Potsatizana naye Hananiya mwana wa Selemiya, ndi Hanuni mwana wacisanu ndi cimodzi wa Salafi, anakonza gawo lina. Potsatizana naye anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya pandunji pa cipinda cace.
31 Potsatizana naye anakonza Malikiya wina wa osula golidi kufikira ku nyumba ya Anetini, ndi ya ocita malonda, pandunji pa cipata ca Hamifikadi, ndi ku cipinda cosanja ca kungondya.
32 Ndi pakati pa cipinda cosanja ca kungondya ndi cipata cankhosa anakonza osula golidi ndi ocita malonda.