Nehemiya 2 BL92

Aritasasta alola Nehemiya akamange linga la Yerusalemu

1 Koma kunacitika mwezi wa Nisana, caka ca makumi awiri ca Aritasasta mfumu pokhala vinyo pamaso pace, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wacisoni pamaso pace ndi kale lonse.

2 Ninena nane mfumu, Nkhope yako nja cisoni cifukwa ninji popeza sudwala? ici si cinthu cina koma cisoni ca mtima. Pamenepo ndinacita mantha akuru.

3 Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kucita cisoni, popeza pali bwinja kumudzi kuli manda a makolo anga, ndi zipata zace zopsereza ndi moto.

4 Ndipo mfumu inati kwa ine, Ufunanji iwe? Pamenepo ndinapemphera Mulungu wa Kumwamba.

5 Ndipo ndinati kwa mfumu, Cikakomera mfumu, ndi mtima wanu ukakomera kapolo wanu, munditumize ku Yuda ku mudzi wa manda a makolo anga, kuti ndiumange.

6 Ninena nane mfumu, irikukhala pansi pamodzi ndi mkazi wace wamkuru, Ulendo wako ngwa nthawi yanji, udzabweranso liti? Ndipo kudakonda mfumu kunditumiza nditaichula nthawi.

7 Ndinanenanso kwa mfumu, Cikakomera mfumu, indipatse akalata kwa ziwanga za tsidya lija la mtsinje, andilole ndipitirire mpaka ndifikira ku Yuda;

8 ndi kalata kwa Asafu wosunga misitu ya mfumu, kuti andipatse mitengo ya mitanda ya ku zipata, za linga liri kukacisi, ndi ya linga la mudzi, ndi ya nyumba imene ndidzalowamo ine. Ndipo mfumu inandipatsa monga mwa dzanja lokoma la Mulungu londikhalira.

9 Ndinafika tsono kwa ziwanga za tsidya lino la mtsinje, ndipo ndinawapatsa akalata a mfumu. Koma mfumu idatumiza apite nane akazembe a nkhondo, ndi apakavalo.

10 Atamva Sanibalati Mhoroni, ndi Tobiya kapoloyo M-amoni, cidawaipira kwakukuru, kuti wadza munthu kuwafunica ana a Israyeli cokoma.

11 Motero ndinafika ku Yerusalemu, ndi kukhalako masiku atatu.

12 Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine coika Mulungu wanga m'mtima mwanga ndicitire Yerusalemu; panalibenso nyama yina nane, koma nyama imene ndinakhalapo.

13 Ndipo ndinaturuka usiku pa cipata ca kucigwa, kumka ku citsime ca cinjoka, ndi ku cipata ca kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zace zothedwa ndi moto.

14 Ndipo ndinapitima kumka ku cipata cacitsime, ndi ku dziwe la mfumu; koma popita nyama iri pansi panga panaicepera.

15 Ndipo ndinakwera usiku kumtsinje, ndi kuyang'ana lingali; ndinabwerera tsono ndi kulowa pa cipata ca kucigwa, momwemo ndinabwereranso.

16 Koma olamulira sanadziwa uko ndinamuka, kapena cocita ine; sindidauzenso kufikira pamenepo Ayuda, kapena ansembe, kapena aufuru, kapena olamulira, kapena otsala akucita nchitoyi.

17 Pamenepo ndinanena nao, Muona coipa m'mene tirimo, kuti Yerusalemu ali bwinja, ndi zipata zace zotentha ndi moto; tiyeni, timange linga la Yerusalemu, tisakhalenso cotonzedwa.

18 Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Cotero anandilimbitsira manja mokoma.

19 Koma Sanibalati Mhoroni, ndi Tobiya kapolo M-amoniyo, ndi Gesemu M-arabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Ciani ici mucicita? Mulikupandukira mfumu kodi?

20 Koma ndinawabwezera mau, ndi kunena nao, Mulungu Wam'mwamba, Iye ndiye adzatilemeza; cifukwa cace ife akapolo ace tidzanyamuka ndi kumanga; koma inu mulibe gawo, kapena ulamuliro, kapena cikumbukilo, m'Yerusalemu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13