1 Ndipo kunali, atamva Sanibalati kuti tinalikumanga lingali, kudamuipira, nakwiya kwakukuru, naseka Ayuda pwepwete.
2 Nanena iye pamaso pa abale ace ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikucitanji Ayuda ofokawa? adzimangire linga kodi? adzapereka nsembe kodi? adzatsiriza tsiku limodzi kodi? adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa?
3 Ndipo Tobiya M-amoni anali naye, nati, Cinkana ici acimanga, ikakwerako nkhandwe, idzagamula linga lao lamiyala.
4 Imvani, Mulungu wathu, popeza tanyozeka ife; muwabwezere citonzo cao pamtu pao, ndi kuwapereka akhale cofunkhidwa m'dziko la ndende;
5 ndipo musakwirira mphulupulu yao, ndi kulakwa kwao kusafafanizike pamaso panu; pakuti anautsa mkwiyo wanu pamaso pa omanga linga.
6 Koma tinamanga lingali, ndi linga lonse linalumikizana kufikira pakati mpakati; popeza mitima ya anthu inalunjika kunchito.
7 Koma kunali, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Aarabu, ndi Aamoni, ndi Aasidodi, kuti makonzedwe a malinga a Yerusalemu anakula, ndi kuti mopasuka mwace munayamba kutsekeka, cidawaipira kwambiri;
8 napangana ciwembu iwo onse pamodzi, kudzathira nkhondo ku Yerusalemu, ndi kucita cisokonezo m'menemo.
9 Koma tinapemphera kwa Mulungu wathu, ndi kuwaikira olindirira usana ndi usiku, cifukwa ca iwowa.
10 Ndipo Ayuda anati, Mphamvu ya osenza akatundu yatha, ndi dothi licuruka, motero sitidzakhoza kumanga lingali.
11 Nati adani athu, Sadzadziwa kapena kuona mpaka talowa pakati pao, ndi kuwapha, ndi kuleketsa nchitoyi.
12 Ndipo kunali, atafika Ayuda okhala pafupi pao ocokera pamalo ponse, anatiuza ife kakhumi, Bwererani kwa ife.
13 Cifukwa cace ndinawaika potera m'kati mwa linga, popenyeka; inde ndinaika anthu monga mwa mabanja ao, akhale nao malupanga ao, nthungo zao, ndi mauta ao.
14 Ndipo ndinapenya, ndinanyamuka, ndinanena kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Musamawaopa iwo; kumbukilani Yehova wamkuru ndi woopsa, ndi kuponyera nkhondo abale anu, ana anu amuna ndi akazi, akazi anu, ndi nyumba zanu.
15 Ndipo kunali, pakumva adani athu kuti cinadziwika nafe, ndi kuti Mulungu adapititsa pacabe uphungu wao, tinabwera tonse kumka kulinga, yense ku nchito yace.
16 Ndipo kuyambira pamenepo gawo lina la anyamata anga anagwira nchito, ndi gawo ina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi maraya acitsulo; ndi akuru anali m'mbuyo mwa nyumba yonse ya Yuda.
17 Iwo omanga linga, ndi iwo osenza katundu, posenza, anacita ali yense ndi dzanja lace lina logwira nchito, ndi lina logwira cida;
18 ndi omanga linga ali yense anamangirira lupanga lace m'cuuno mwace, nagwira nchito motero. Ndipo woomba lipenga anali ndi ine.
19 Ndipo ndinati kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Nchito ndiyo yocuruka ndi yacitando, ndi ife tiri palace palace palingapo, yense azana ndi mnzace;
20 pali ponse mukumva mau a lipenga, musonkhanire komweko kwa ife; Mulungu wathu adzatigwirira nkhondo.
21 Momwemo tinalikugwira nchito; gawo lina la iwo linagwira nthungo kuyambira mbanda kuca mpaka zaturuka nyenyezi.
22 Ndinanenanso kwa anthu nthawi yomweyi, Ali yense agone m'Yerusalemu pamodzi ndi mnyamata wace, kuti atilindirire usiku, ndi kugwira nchito usana.
23 Ndipo ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, angakhale amuna olindirira onditsata ine, nnena mmodzi yense wa ife anabvula zobvala zace, yense anapita ndi cida cace kumadzi.