1 Ndipo akuru anthu anakhala m'Yerusalemu; anthu otsala omwe anacita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale m'Yerusalemu, mudzi wopatulika, ndi asanu ndi anai a khumi m'midzi yina.
2 Ndipo anthu anadalitsa amuna onse a akudzinenera mwaufulu kuti adzakhala m'Yerusalemu.
3 Awa tsono ndi akulu a dziko okhala m'Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa colowa cace m'midzi mwao, ndiwo Israyeli, ansembe, ndi Alevi, ndi Anetini, ndi ana a akapolo a Solomo.
4 Ndipo m'Yerusalemu munakhala ena a ana a Yuda ndi a ana a Benjamini. Mwa ana a Yuda: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalaleli, wa ana a Perezi;
5 ndi Maaseya mwana wa Baruki, mwana wa Koloze, mwana wa Huzaya, mwana wa Adaya, mwana wa Yoyaribi, mwana wa Zekariya, mwana wa Msiloni.
6 Ana onse a Perezi okhala m'Yerusalemu ndiwo ngwazi mazana anai mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi atatu.
7 Ndi ana a Benjamini ndi awa: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Yoedi, mwana wa Pedaya, mwana Wa Kolaya, mwana wa Maseya, mwana wa Itiyeli, mwana wa Yesaya.
8 Ndi wotsatananaye Gabai, Salai, mazana asanu ndi anai mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.
9 Ndi Yoeli mwana wa Zikiri ndiye woyang'anira wao, ndi Yuda mwana wa Hasenuwa ndiye wothandizana naye, poyang'anira mudzi.
10 Mwa ansembe: Yedaya mwana wa Yoyaribi, Yakini,
11 Seraya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubu mtsogoleri wa m'nyumba ya Mulungu;
12 ndi abale ao ocita nchito ya m'nyumbayi ndiwo mazana asanu ndi atatu mphambu makumi awiri kudza awiri; ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amzi, mwana wa Zekariya, mwana: wa Pasuru, mwana wa Malikiya;
13 ndi abale ace akulu a nyumba za makolo awiri mphambu makumi anai kudza awiri, ndi Amasai mwana wa Azareli, mwana wa Azai, mwana wa Mesilimoti, mwana wa Imeri;
14 ndi abale ao, ngwazi zamphamvu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu; ndi woyang'anira wao ndiye Zabidiyeli mwana wa Hagedolimu.
15 Ndi mwa Alevi: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, mwana wa Buni;
16 ndi Sabetai, ndi Yozabadi, mwa akuru a Alevi, anayang'anira nchito za pabwalo za nyumba ya Mulungu;
17 ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkuru wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ace, ndi Abida mwana wa Samua, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.
18 Alevi onse m'mudzi wopatulikawo ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu kudza anai.
19 Ndi odikira: Akubu, Talimoni, ndi abale ao akulindira pazipata, ndiwo zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.
20 Ndi Aisrayeli otsala, ndiwo ansembe ndi Alevi, anakhala m'midzi yonse ya Yuda, yense m'colowa cace.
21 Koma Anetini anakhala m'Ofeli, ndi Ziya, ndi Gisipa anali oyang'anira Anetini.
22 Ndipo woyang'anira wa Alevi m'Yerusalemu ndiye Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika; mwa ana a Asafu oyimbira ena anayang'anira nchito ya m'nyumba ya Mulungu.
23 Pakuti mfumu inalamulira za iwowa, naikira oyimbira cowathandiza, yense cace pa tsiku lace.
24 Ndi Petatiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa mirandu yonse ya anthuwo.
25 Ndi ana ena a Yuda anakhala m'midzi ya ku minda yao, m'Kiriyati Ariba ndi miraga yace, ndi m'Diboni ndi miraga yace, ndi m'Yekabizeeli ndi midzi yace,
26 ndi m'Yesuwa, ndi m'Molada, ndi Betepeleti,
27 ndi m'Hazarisuala, ndi m'Beereseba ndi miraga yace,
28 ndi m'Zikilaga, ndi m'Mekona ndi miraga yace,
29 ndi m'Enirimoni, ndi m'Zora, ndi m'Yarimuti,
30 Zanowa, Adulamu ndi midzi yao, Lakisi ndi minda yace, Azeka ndi miraga yace. Ndipo anamanga misasa kuyambira ku Beereseba mpaka cigwa ca Hinomu.
31 Ana a Benjamini omwe, kuyambira ku Geba pa Mikimasi, ndi Aiya, ndi pa Beteli ndi miraga yace,
32 pa Anatoti, Nobi, Ananiya,
33 Hazori, Rama, Gitaimu,
34 Hadidi, Zeboimu, Nebalati,
35 Lodi, ndi Ono, cigwa ca amisiri.
36 Ndi magawo a Levi anakhala ena ku Yuda, ndi ena ku Benjamini.