1 Okomera cizindikilo tsono ndiwo Nehemiya, Tirisata mwana wa Hakaliya, ndi Zedekiya,
2 Seraya, Agariya, Yeremiya,
3 Pasuri, Amariya, Malikiya,
4 Hatusi, Sebaniya, Maluki,
5 Harimu, Meremoti, Obadiya,
6 Danieli, Ginetoni, Baruki,
7 Mesulamu, Abiya, Miyamini,
8 Maaziya, Biligai, Semaya, ndiwo ansembe.
9 Ndi Alevi ndiwo Yesuwa mwana wa Azaniya, Binui wa ana a Henadadi, Kadiniyeli;
10 ndi abale ao: Sebaniya, Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani,
11 Mika, Rehobo, Hasabiya,
12 Zakuri, Serebiya, Sebaniya,
13 Hodiya, Bani, Beninu.
14 Akuru a anthu: Parosi, Patati, Moabu, Elamu, Zatu, Bani,
15 Buni, Azigadi, Bebai,
16 Adoniya, Bigivai, Adini,
17 Ateri, Hezekiya, Azuri,
18 Hodiya, Hasumu, Bezai,
19 Harifi, Anatoti, Nobai,
20 Magipiasi, Mesulamu, Heziri,
21 Mesezabele, Zadoki, Yaduwa,
22 Pelatiya, Hanani, Ananiya,
23 Hoseya, Hananiya, Hasubi,
24 Halohesi, Pila, Sobeki,
25 Rehumu, Hasabina, Maaseya,
26 ndi Ahiya, Hanani, Anani,
27 Maluki, Harimu, Baana.
28 Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oyimbira, Anetini, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m'dziko kutsata cilamulo ca Mulugu, akazi ao, ana ao amuna ndi akazi, yense wodziwa ndi wozindikira,
29 amenewa anaumirira abale ao, omveka ao, nalowa m'temberero ndi lumbiro, kuti adzayenda m'cilamulo ca Mulungu anacipereka Mose mtumiki wa Mulungu, ndi kuti adzasunga ndi kucita zonse atilamulira Yehova Ambuye wathu, ndi maweruzo ace, ndi malemba ace;
30 ndi kuti sitidzapereka ana athu akazi kwa mitundu ya anthu a m'dziko, kapena kutengera ana athu amuna ana ao akazi;
31 ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, dzuwa la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao dzuwa la Sabata, kapena dzuwa lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka caka cacisanu ndi ciwiri ndi mangawa ali onse.
32 Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka caka ndi caka limodzi la magawo atatu a sekeli ku nchito ya nyumba ya Mulungu wathu;
33 kuliperekera mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israyeli zoipa, ndi nchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu.
34 Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a copereka ca nkhuni, kubwera nazo ku nyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika caka ndi caka, kuzisonkha pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'cilamulo;
35 ndi kubwera nazo zipatso zoyamba za nthaka, ndi zoyamba za zipatso zonse za mtengo uli wonse caka ndi caka, ku nyumba ya Yehova;
36 ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'cilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo ku nyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu;
37 ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uli wonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, ku zipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzi limodzi la magawo khumi m'midzi yonse yolima ife.
38 Ndipo wansembe mwana wa Aroni azikhala ndi Alevi, polandira Alevi limodzi limodzi la magawo khumi; ndi Alevi azikwera nalo limodzi la magawo khumi mwa limodzi limodzi la magawo khumi ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda, ku nyumba ya cuma.
39 Pakuti ana a Israyeli ndi ana a Levi, azibwera nayo nsembe yokweza yatirigu, ndi yavinyo ndi yamafuta, kuzipinda kuli zipangizo za malo opatulika, ndi ansembe akutumikira, ndi odikira, ndi oyimbira; kuti tisasiye nyumba ya Mulungu wathu.