Nehemiya 9 BL92

Msonkhano wa kusala ndi kupemphera

1 Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi uno ana a Israyeli anasonkhana ndi kusala, ndi kubvala ciguduli, ndipo anali ndi pfumbi.

2 Nadzipatula a mbumba ya Israyeli kwa alendo onse, naimirira, naulula zocimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao.

3 Naimima poima pao, nawerenga m'buku la cilamulo ca Yehova Mulungu wao limodzi la magawo anai a tsiku; ndi limodzi la magawo anai anaulula, napembedza Yehova Mulungu wao.

4 Pamenepo anaimirira pa ciunda ca Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyeli, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, napfuula ndi mau akuru kwa Yehova Mulungu wao.

5 Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyeli, Buni, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petatiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu ku nthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa cilemekezo ndi ciyamiko conse.

6 Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse ziri pomwepo, nyanja ndi zonse ziri m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu la kumwamba lilambira Inu.

7 Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumturutsa m'Uri wa Akasidi, ndi kumucha dzina lace Abrahamu;

8 ndipo munampeza mtima wace wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zace; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama.

9 Ndipo munapenya msauko wa makolo athu m'Aigupto, nimunamva kupfuula kwao ku Nyanja Yofiira,

10 nimunacitira zizindikilo ndi zodabwiza Farao ndi akapolo ace onse, ndi anthu onse a m'dziko lace; popeza munadziwa kuti anawacitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.

11 Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.

12 Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo.

13 Munatsikiranso pa phiri la Sinai, nimunalankhula nao mocokera m'Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi cilamulo coona, malemba, ndi malamulo okoma;

14 ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi cilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;

15 ndi mkate wocokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi oturuka m'thanthwe munawaturutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.

16 Koma iwo ndi makolo athu anacita modzikuza, naumitsa khosi lao, osamvera malamulo anu,

17 nakana kumvera, osakumbukilansozodabwiza zanu munazicita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m'kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kumka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wacisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wocuruka cifundo; ndipo simunawasiya.

18 Ngakhale apa atadzipangira mwana wa ng'ombe woyenga, nati, Suyu Mulungu wako anakukweza kucokera ku Aigupto, nacita zopeputsa zazikuru;

19 koma Inu mwa nsoni zanu zazikuru simunawasiya m'cipululu; mtambo woti njo sunawacokera usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.

20 Munawapatsanso mzimu wanu wokoma kuwalangiza, ndipo simunawamana mana anu pakamwa pao; munawapatsanso madzi pa ludzu lao.

21 Ndipo munawalera zaka makumi anai m'cipululu, osasowa kanthu iwo; zobvala zao sizinatha, ndi mapazi ao sanatupa.

22 Munawapatsanso maufumu, ndi mitundu ya anthu, nimunawagawa m'madera, motero analandira likhale lao lao dziko la Sihoni, ndilo dziko la mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basana.

23 Ana aonso munawacurukitsa monga nyenyezi za m'mwamba, nimunawalowetsa m'dziko mudalinena kwa makolo ao, alowemo likhale lao lao.

24 Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale lao lao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m'dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m'dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m'dziko, kuti acite nao cifuniro cao.

25 Ndipo analanda midzi yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zao zao nyumba zodza la ndi zokoma ziri zonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda yaazitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukuru.

26 Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya cilamulo canu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwacitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nacita zopeputsa zazikuru.

27 Cifukwa cace munawapereka m'dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anapfuula kwa Inu, ndipo munamva m'Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m'dzanja la adani ao.

28 Koma atapumula, anabwereza kucita coipa pamaso panu; cifukwa cace munawasiya m'dzanja la adani ao amene anacita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kupfuula kwa Inu, munamva m'Mwamba ndi kuwapulumutsa kawiri kawiri, monga mwa cifundo canu;

29 ndipo munawacitira umboni, kuti muwabwezerenso ku cilamulo canu; koma anacita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anacimwira malamulo anu (amene munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera.

30 Koma munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwacitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu, koma sanamvera; cifukwa cace munawapereka m'dzanja la mitundu ya anthu a m'dziko.

31 Ndipo mwa nsoni zanu zocuruka simunawatha, kapena kuwataya; popeza Inu ndinu Mulungu wa cisomo ndi cifundo.

32 Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkuru, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi cifundo, asacepe pamaso panu mabvuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akuru athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asuri, mpaka lero lino.

33 Koma Inu ndinu wolungama mwa zonse zatigwera; pakuti mwacita zoona, koma ife tacita coipa;

34 ndi mafumu athu, akuru athu, ansembe athu, ndi makolo athu, sanasunga cilamulo canu, kapena kumvera malamulo anu, ndi mboni zanu, zimene munawacitira umboni nazo.

35 Popeza sanatumikira Inu m'ufumu wao, ndi m'ubwino wanu wocuruka umene mudawapatsa, ndi m'dziko lalikuru ndi la zonona mudalipereka pamaso pao, ndipo sanabwerera kuleka nchito zao zoipa.

36 Tapenyani, ife lero ndife akapolo, ndi dzikoli mudalipereka kwa makolo athu kudya zipatso zace ndi zokoma zace, taonani, ife ndife akapolo m'menemo.

37 Ndipo licurukitsira mafumu zipatso zace, ndiwo amene munawaika atiweruze, cifukwa ca zoipa zathu; acitanso ufumu pa matupi athu, ndi pa zaweta zathu, monga umo akonda; ndipo ife tisauka kwakukuru.

38 Ndipo mwa ici conse ticita pangano lokhazikika, ndi kulilemba, ndi akulu athu, Alevi athu, ndi ansembe athu, alikomera cizindikilo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13