Nehemiya 8 BL92

Ezara awerengera anthu buku la cilamulo

1 Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi ku khwalala liri ku cipata ca kumadzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la cilamulo ca Mose, cimene Yehova adalamulira Israyeli.

2 Ndipo Ezara wansembe anabwera naco cilamulo pamaso pa msonkhano, ndiwo amuna ndi akazi, ndi yense wakumva ndi kuzindikira tsiku loyamba la mwezi wacisanu ndi ciwiri.

3 Nawerenga m'menemo pa khwalala liri ku cipata ca kumadzi kuyambira mbanda kuca kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anacherera khutu buku la cilamulo.

4 Ndipo Ezara mlembi anaima pa ciunda ca mitengo adacimangira msonkhanowo; ndi pambali: pace padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseya, ku dzanja lamanja lace; ndi ku dzanja lamanzere Pedaya, ndi Misayeli, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.

5 Ndipo Ezara anafunyulula bukulo pamaso pa anthu onse, popeza iye anasomphokera anthu onse; ndipo polifunyulula anthu onse ananyamuka.

6 Pamenepo Ezara analemekeza Yehova Mulungu wamkuru. Nabvomereza anthu onse, ndi kuti, Amen, Amen; nakweza manja ao, nawerama, nalambira Yehova nkhope zao pansi.

7 Ndi Yesuwa, ndi Bani, ndi Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodayi, Maaseya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani, Pelaya, ndi Alevi, anadziwitsa anthu cilamuloco; ndi anthu anali ciriri pamalo pao,

8 Nawerenga iwo m'buku m'cilamulo ca Mulungu momveka, natanthauzira, nawazindikiritsa cowerengedwaco.

9 Ndipo Nehemiya, ndiye kazembe, ndi Ezara wansembe mlembiyo, ndi Alevi ophunzitsa anthu, ananena ndi anthu onse, Lero ndilo lopatulikira Yehova Mulungu wanu, musamacita maliro, musamalira misozi. Popeza anthu onse analira misozi pakumva mau a cilamulo.

10 Nanena naonso, Mukani mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lace iye amene sanamkonze ratu kanthu; cifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamacita cisoni; pakuti cimwemwe ca Yehova ndico mphamvu yanu.

11 Ndipo Alevi anatontholetsa anthu onse, ndi kuti, Khalani muli cete; pakuti lero ndi lopatulika; musamacita cisoni.

12 Napita anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukuru; popeza anazindikira mau amene adawafotokozera.

Madyerero a misasa

13 Ndipo m'mawa mwace akuru a nyumba za makolo a anthu onse, ansembe, ndi Alevi anasonkhana pamodzi kwa Ezara mlembi, kuti atole nzeru za mau a cilamulo.

14 Napeza munalembedwa m'cilamulo kuti Yehova analamulira ndi Mose, kuti ana a Israyeli azikhala m'misasa pa madyerero a mwezi wacisanu ndi ciwiri,

15 ndi kuti azilalikira ndi kumveketsa m'midzi mwao monse ndi m'Yerusalemu, ndi kuti, Muziturukira kuphiri, ndi kutengako nthambi za azitona, ndi nthambi za mitengo yamafuta, ndi nthambi za mitengo yamcisu, ndi zinkhwamba za migwalangwa, ndi nthambi za mitengo zothonana, kumanga nazo misasa monga munalembedwa.

16 Naturuka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yace, ndi m'mabwalo ao, ndi m'mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la cipata ca kumadzi, ndi pa khwalala la cipata ca Efraimu.

17 Ndi msonkhano wonse wa iwo oturuka m'ndende anamanga misasa, nakhala m'misasamo; pakuti ciyambire masiku a Yesuwa mwana wa Nuni kufikira tsiku lija ana a Israyeli sanatero. Ndipo panali cimwemwe cacikuru.

18 Anawerenganso m'buku la cilamulo ca Mulungu tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza. Nacita madyerero masiku asanu ndi awiri; ndi tsiku lacisanu ndi citaru ndilo msonkhano woletsa, monga mwa malemba.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13