1 Pamenepo panamveka kulira kwakukuru kwa anthu ndi akazi ao kudandaula pa abale ao Ayuda.
2 Popeza panali ena akuti, Ife, ana athu amuna ndi akazi, ndife ambiri; talandira tirigu, kuti tidye tikhale ndi moyo.
3 Panali enanso akuti, Tirikupereka cikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa ndi nyumba zathu; kuti tilandire tirigu cifukwa ca njalayi.
4 Panali enanso akuti, Takongola ndarama za msonkho wa mfumu; taperekapo cikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa.
5 Koma tsopano thupi lathu likunga thupi la abale athu, ana athu akunga ana ao; ndipo taonani, titengetsa ana athu amuna ndi akazi akhale akapolo, ndi ana athu akazi ena tawatengetsa kale; ndipo tiribe ife mphamvu ya kucitapo kanthu; ndi minda yathu, ndi minda yathu yampesa, nja ena.
6 Ndipo pakumva kulira kwao, ndi mau ao, kunandiipira kwambiri.
7 Pamenepo mtima wanga unandipangira; ndipo ndinatsutsana nao aufuru ndi olamulira, ndi kunena nao, Mukongoletsa mwa phindu yense kwa mbale wace. Ndipo ndinasonkhanitsa msonkhano waukuru wakuwatsutsa.
8 Ndipo ndinanena, nao, Ife monga umo tinakhoza, tinaombola abale athu Ayuda ogulitsidwa kwa amitundu; ndipo kodi inu mukuti mugulitse abale anu, kapena tiwagule ndi ife? Pamenepo anakhala du, nasowa ponena.
9 Ndinatinso, Cinthu mucitaci si cokoma ai; simuyenera kodi kuyenda m'kuopa Mulungu wathu, cifukwa ca mnyozo wa amitundu, ndiwo adani athu?
10 Kodi ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, tiwakongoletsa ndarama ndi tirigu mwa phindu? Ndikupemphani, tileke phindu ili.
11 Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao yaazitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndarama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa.
12 Pamenepo anati, Tidzawabwezera osawalipitsa kanthu, tidzacita monga momwe mwanena. Pamenepo ndinaitana ansembe, ndi kuwalumbiritsa, kuti adzacita monga mwa mau awa.
13 Ndinakutumulanso maraya anga, ndi kuti, Mulungu akutumule momwemo munthu yense wosasunga mau awa, ku nyumba yace, ndi ku nchito yace; inde amkutumule momwemo, namtayire zace zonse. Ndi msonkhano wonse unati, Amen, nalemekeza Yehova. Ndipo anthu anacita monga mwa mau awa.
14 Ndipo ciyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m'dziko la Yuda; kuyambira caka ca makumi awiri kufikira caka ca makumi atatu mphambu ziwiri ca Aritasasta mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadya cakudya ca kazembe.
15 Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakale anyamata ao anacita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, cifukwa ca kuopa Mulungu.
16 Ndiponso ndinalimbikira nchito ya linga ili, ngakhale dziko sitinaligula, ndi anyamata anga onse anasonkhanira nchito komweko.
17 Panalinso podyera ine Ayuda ndi olamulira amuna zana limodzi; mphambu makumi asanu, pamodzi ndi iwo akutidzera kucokera kwa amitundu otizinga.
18 Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng'ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundu mitundu; cinkana conseci sindinafunsira cakudya ca kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo.
19 Mundikumbukire Mulungu, zindikomere zonse ndinacitira anthu awa.