3 Awa tsono ndi akulu a dziko okhala m'Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa colowa cace m'midzi mwao, ndiwo Israyeli, ansembe, ndi Alevi, ndi Anetini, ndi ana a akapolo a Solomo.
4 Ndipo m'Yerusalemu munakhala ena a ana a Yuda ndi a ana a Benjamini. Mwa ana a Yuda: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalaleli, wa ana a Perezi;
5 ndi Maaseya mwana wa Baruki, mwana wa Koloze, mwana wa Huzaya, mwana wa Adaya, mwana wa Yoyaribi, mwana wa Zekariya, mwana wa Msiloni.
6 Ana onse a Perezi okhala m'Yerusalemu ndiwo ngwazi mazana anai mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi atatu.
7 Ndi ana a Benjamini ndi awa: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Yoedi, mwana wa Pedaya, mwana Wa Kolaya, mwana wa Maseya, mwana wa Itiyeli, mwana wa Yesaya.
8 Ndi wotsatananaye Gabai, Salai, mazana asanu ndi anai mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.
9 Ndi Yoeli mwana wa Zikiri ndiye woyang'anira wao, ndi Yuda mwana wa Hasenuwa ndiye wothandizana naye, poyang'anira mudzi.