16 wa Ido, Zekariya; wa Ginetoni, Mesulamu;
17 wa Abiya, Zikiri; wa Minyamini, wa Moadiya, Pilitai;
18 wa Biliga, Samura; wa Semaya, Yehonatani;
19 ndi wa Yoyaribi, Matani; wa Yedaya, Uzi;
20 wa Salai, Kalai; wa Amoki, Eberi;
21 wa Hilikiya, Hasabiya; wa Yedaya, Netaneli.
22 M'masiku a Ehasibi, Yoyada, Yohanana, ndi Yoduwa, Alevi analembedwa akuru a nyumba za makolo; ansembe omwe, mpaka ufumu wa Dariyo wa ku Perisiya.