40 Atatero, magulu awiriwo a iwo oyamikira anaima m'nyumba ya Mulungu, ndipo ine ndi limodzi la magawo awiri a olamulira pamodzi ndi ine;
41 ndi ansembe, Eliakimu, Maaseya, Minyamini, Mikaya, Elioenai, Zekariya, ndi Hananiya, ali nao malipenga;
42 ndi Maaseya, ndi Semaya, ndi Eleazara, ndi Uzi, ndi Yehohanana, ndi Malikiya, ndi Elamu, ndi Ezeri. Ndipo oyimbira anayimbitsa Yeziraya ndiye woyang'anira wao.
43 Ndipo anaphera nsembe zambiri tsiku lija, nasekerera; pakuti Mulungu anawakondweretsa ndi cimwemwe cacikuru; ndi akazi omwe ndi ana anakondwera; ndi cikondwerero ca Yerusalemu cinamveka kutali.
44 Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za cuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzi limodzi la magawo khumi, kulonga m'mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi cilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi lakuimirirako.
45 Ndipo iwo anasunga udikiro wa Mulungu wao, ndi udikiro wa mayeretsedwe; momwemonso oyimbira ndi odikira, monga mwa lamulo la Davide ndi la Solomo mwana wace.
46 Pakuti m'masiku a Davide ndi Asafu kalelo kunali mkuru wa oyimbira, ndi wa nyimbo zolemekeza ndi zoyamikira Mulungu.