1 Tsiku lomwelo anawerenga m'buku la Mose m'makutu a anthu, napeza m'menemo kuti Aamoni ndi Amoabu asalowe mu msonkhano wa Mulungu ku nthawi yonse;
2 popeza sanawacingamira ana a Israyeli ndi cakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso.
3 Ndipo kunali, atamva cilamuloco, anasiyanitsa pa Israyeli anthu osokonezeka onse.
4 Cinkana ici, Eliasibu wansembe, woikidwa asunge zipinda za nyumba ya Mulungu wathu, anacita cibale ndi Tobiya,