15 Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m'coponderamo dzuwa la Sabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa aburu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza ziri zonse, zimene analowa nazo m'Yerusalemu dzuwa la Sabata, ndipo ndinawacitira umboni wakuwatsutsa tsikuti anagulitsa zakudya.
16 Anakhalanso m'menemo a ku Turo, obwera nazo nsomba, ndi malonda ali onse, nagulitsa dzuwa la Sabata kwa ana a Yuda ndi m'Yerusalemu.
17 Pamenepo ndinatsutsana nao aufulu a Yuda, ndinanena nao, Cinthu canji coipa ici mucicita, ndi kuipsa naco dzuwa la Sabata?
18 Sanatero kodi makolo anu, ndipo Mulungu wathu anatifikitsira ife ndi mudzi uno coipa ici conse? koma inu muonjezera Israyeli mkwiyo pakuipsa Sabata.
19 Ndipo kunali, kukadayamba cizirezire pa zipata za Yerusalemu, losafika Sabata, ndinawauza atseke pamakomo; ndinawauzanso kuti asatsegulepo, koma litapita Sabata ndipo; ndipo ndinaimika anyamata anga ena pazipata, kuti pasalowe katundu dzuwa la Sabata.
20 Momwemo eni malonda ndi ogulitsa malonda ali onse, anagona kunja kwa Yerusalemu kamodzi kapena kawiri.
21 Koma ndinawacima umboni wakuwatsutsa, ndinanena nao, Mugoneranji pafupi pa linga? mukateronso ndikuthirani manja. Kuyambira pomwepo sanafikanso pa Sabata.