2 popeza sanawacingamira ana a Israyeli ndi cakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso.
3 Ndipo kunali, atamva cilamuloco, anasiyanitsa pa Israyeli anthu osokonezeka onse.
4 Cinkana ici, Eliasibu wansembe, woikidwa asunge zipinda za nyumba ya Mulungu wathu, anacita cibale ndi Tobiya,
5 namkonzera cipinda cacikuru, kumene adasungira kale zopereka za ufa, libano, ndi zipangizo, ndi limodzi limodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamutidwira Alevi, ndi oyimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe.
6 Koma pocitika ici conse sindinakhala ku Yerusalemu; pakuti caka ca makumi atatu ndi caciwiri ca Aritasasta mfumu ya Babulo ndinafika kwa mfumu, ndipo atapita masiku ena ndinapempha mfumu indilole;
7 ndipo ndinafika ku Yerusalemu, ndi kuzindikira coipa anacicita Eliasibu, cifukwa ca Tobiya, ndi kumkonzera cipinda m'mabwalo a nyumba ya Mulungu.
8 Ndipo ndinaipidwa naco kwambiri, motero ndinataya kubwalo akatundu onse a m'nyumba ya Tobiya, kuwacotsa m'cipindamo.