3 Panali enanso akuti, Tirikupereka cikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa ndi nyumba zathu; kuti tilandire tirigu cifukwa ca njalayi.
4 Panali enanso akuti, Takongola ndarama za msonkho wa mfumu; taperekapo cikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa.
5 Koma tsopano thupi lathu likunga thupi la abale athu, ana athu akunga ana ao; ndipo taonani, titengetsa ana athu amuna ndi akazi akhale akapolo, ndi ana athu akazi ena tawatengetsa kale; ndipo tiribe ife mphamvu ya kucitapo kanthu; ndi minda yathu, ndi minda yathu yampesa, nja ena.
6 Ndipo pakumva kulira kwao, ndi mau ao, kunandiipira kwambiri.
7 Pamenepo mtima wanga unandipangira; ndipo ndinatsutsana nao aufuru ndi olamulira, ndi kunena nao, Mukongoletsa mwa phindu yense kwa mbale wace. Ndipo ndinasonkhanitsa msonkhano waukuru wakuwatsutsa.
8 Ndipo ndinanena, nao, Ife monga umo tinakhoza, tinaombola abale athu Ayuda ogulitsidwa kwa amitundu; ndipo kodi inu mukuti mugulitse abale anu, kapena tiwagule ndi ife? Pamenepo anakhala du, nasowa ponena.
9 Ndinatinso, Cinthu mucitaci si cokoma ai; simuyenera kodi kuyenda m'kuopa Mulungu wathu, cifukwa ca mnyozo wa amitundu, ndiwo adani athu?