3 Ndinanenanso nao, Asatsegule pa zipata za Yerusalemu lisanafunde dzuwa; ndi poimirira odikira atseke pazipata, nimuzipiringidze, nimuike alonda mwa iwo okhala m'Yerusalemu, yense polindirira pace, yense pandunji pa nyumba yace.
4 Mudziwo tsono ndi wacitando, ndi waukuru; koma anthu anali m'mwemo ngowerengeka, nyumba zomwe sizinamangike.
5 Ndipo Mulungu wanga anaika m'mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufuru, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa cibadwidwe cao. Ndipo ndinapeza buku la cibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m'mwemo.
6 Ana a dziko amene anakwera kucokera kundende a iwo adatengedwa ndende, amene Nebukadinezara mfumu ya Babulo adawatenga, anabwera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, yense ku mudzi wace, ndi awa:
7 ndiwo amene anadza ndi Zerubabele: Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Moredekai, Bilisani, Misiperete, Bigivai, Nehumu, Baana. Mawerengedwe a amuna a anthu Aisrayeli ndiwo:
8 ana a Parosi zikwi ziwiri mphambu zana limodzi kudza makumi asanu ndi awiri.
9 Ana a Sefatiya, mazana atatu mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.