15 ndi kuti azilalikira ndi kumveketsa m'midzi mwao monse ndi m'Yerusalemu, ndi kuti, Muziturukira kuphiri, ndi kutengako nthambi za azitona, ndi nthambi za mitengo yamafuta, ndi nthambi za mitengo yamcisu, ndi zinkhwamba za migwalangwa, ndi nthambi za mitengo zothonana, kumanga nazo misasa monga munalembedwa.
16 Naturuka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yace, ndi m'mabwalo ao, ndi m'mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la cipata ca kumadzi, ndi pa khwalala la cipata ca Efraimu.
17 Ndi msonkhano wonse wa iwo oturuka m'ndende anamanga misasa, nakhala m'misasamo; pakuti ciyambire masiku a Yesuwa mwana wa Nuni kufikira tsiku lija ana a Israyeli sanatero. Ndipo panali cimwemwe cacikuru.
18 Anawerenganso m'buku la cilamulo ca Mulungu tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza. Nacita madyerero masiku asanu ndi awiri; ndi tsiku lacisanu ndi citaru ndilo msonkhano woletsa, monga mwa malemba.