1 Pemphani kwa Yehova mvula, m'nyengo ya mvula ya masika, kwa Yehova wolenga mphezi; ndipo adzawapatsa mibvumbi ya mvula, kwayense zophukira kuthengo.
2 Pakuti aterafi anena zopanda pace, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto acabe, asangalatsa nazo zopanda pace; cifukwa cace ayendayenda ngati nkhosa, azunzika popeza palibe mbusa.
3 Mkwiyo wanga wayakira abusa, ndipo ndidzalanga atonde; pakuti Yehova wa makamu adzazonda zoweta zace, ndizo nyumba ya Yuda, nadzaziika ngati kavalo wace waulemerero kunkhondo.
4 Kwa iye kudzafuma mwala wa kungondya, kwa iye msomali, kwa iye uta wankhondo, kwa iye osautsa onse pamodzi.